["Nyimbo yoposa, ndiyo ya Solomoni.","Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m'kamwa mwake;pakuti chikondi chako chiposa vinyo.","Mafuta ako anunkhira bwino;dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa;chifukwa chake anamwali akukonda.","Undikoke; tikuthamangire;mfumu yandilowetsa m'zipinda zake:Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe.Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo:Akukonda molungama.","Wakuda ine, koma wokongola,ana akazinu a ku Yerusalemu,ngati mahema a Kedara,ngati nsalu zotchinga za Solomoni.","Musayang'ane pa ine, pakuti ndada,pakuti dzuwa landidetsa.Ana amuna a amai anandikwiyira,anandisungitsa minda yamipesa;koma munda wangawanga wamipesa sindinausunga.","Ndiuze, iwe amene moyo wanga ukukonda,umaweta kuti gulu lako?Umaligonetsa kuti pakati pa usana?Pakuti ndikhalirenji ngati wosocherapambali pa magulu a anzako?","Ngati sudziwa, mkaziwe woposa kukongola,dzituluka kukalondola bande la gululo,nukawete anaambuzi zako pambali pa mahema a abusa.","Ndakulinganiza, wokondedwa wanga mnyamatawe,ngati akavalo a magaleta a Farao.","Masaya ako akongola ndi nkhata zatsitsi,ndi khosi lako ndi zinganga za mkanda wonyezimira.","Tidzakupangira nkhata zagolidendi njumu zasiliva.","Pokhala mfumu podyera pake,narido wanga ananunkhira.","Wokondedwa wanga mnyamatayoali kwa ine ngati thumba la mure,logona pakati pa mawere anga.","Wokondedwa wanga ali kwa inengati chipukutu cha maluwa ofiiram'minda yamipesa ya ku Engedi.","Taona, wakongolatu, bwenzi langa;namwaliwe taona, wakongola,maso ako akunga a nkhunda.","Taona, wakongolatu, bwenzi langa,mnyamatawe, inde, wakongoletsa;pogona pathu mpa msipu.","Mitanda ya nyumba zathu nja mikungudza,ndi mapaso athu nga mlombwa."]