["Mwenzi utakhala ngati mlongo wanga,woyamwa pa bere la amai!Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona;osandinyoza munthu.","Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m'nyumba ya amai,kuti andilange mwambo;ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa,ndi madzi a makangaza anga.","Dzanja lamanzere lake akadanditsamiritsa kumutu,lamanja lake ndi kundifungatira.","Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,muutsiranji, mugalamutsiranji chikondi,chisanafune mwini.","Ndaniyu achokera kuchipululu,alikutsamira bwenzi lake?Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe:Pomwepo amai ako anali mkusauka nawe,pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.","Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro,nundikhomenso chizindikiro pamkono pako;pakuti chikondi chilimba ngati imfa;njiru imangouma ngati manda:Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto,ngati mphezi ya Yehova.","Madzi ambiri sangazimitse chikondi,ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola:Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yakengati sintho la chikondi,akanyozedwa ndithu.","Tili ndi mlongwathu wamng'ono,alibe mawere;timchitirenji mlongo wathutsiku lokhoma unkhoswe wake?","Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva:Ngati ndiye chitseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza.","Ndine khoma, mawere anga akunga nsanja zake:Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.","Solomoni anali ndi munda wamipesa ku Baala-Hamoni;nabwereka alimi mundawo;yense ambwezere ndalama chikwi chifukwa cha zipatso zake.","Koma munda wanga wamipesa,uli pamaso panga ndiwo wangatu;nacho chikwicho, Solomoni iwe,koma olima zipatso zake azilandira mazana awiri.","Namwaliwe wokhala m'minda,anzako amvera mau ako:Nanenanso undimvetse.","Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga,dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawalapa mapiri a mphoka."]