["Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni.","Dengu limodzi linali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kucha; ndipo dengu limodzi linali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.","Ndipo Yehova anati kwa ine, Kodi uona chiyani, Yeremiya? Ndipo ndinati, Nkhuyu, nkhuyu zabwino, nzabwino ndithu; zoipazo nzoipa ndithu, zosadyeka poti nzoipa.","Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,","Chifukwa Yehova, Mulungu wa Israele, atero, Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira am'nsinga a Yuda, amene ndawachotsera m'malo muno kunka kudziko la Ababiloni, kuwachitira bwino.","Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwachitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso kudziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzala, osawazula iwo.","Ndipo ndidzapatsa iwo mtima wakundidziwa, kuti ndine Yehova, nadzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao; pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao.","Ndipo monga nkhuyu zoipa, zosadyeka, poti nzoipa; ntheradi atero Yehova, Chomwecho ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi akulu ake, ndi otsala a m'Yerusalemu, amene atsala m'dziko ili, ndi amene akhala m'dziko la Ejipito.","Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m'mene ndidzawapirikitsiramo.","Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi chaola mwa iwo, mpaka athedwa m'dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo ao."]