["Lipenga kukamwa kwako. Akudza ngati chiombankhanga, kulimbana ndi nyumba ya Yehova; chifukwa analakwira chipangano changa, napikisana nacho chilamulo changa.","Adzafuulira kwa Ine, Mulungu wanga, ife Aisraele tikudziwani.","Israele wachitaya chokoma, mdani adzamlondola.","Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe.","Mwanawang'ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti?","Pakuti ichi chomwe chafumira kwa Israele; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwanawang'ombe wa Samariya adzaphwanyikaphwanyika.","Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza.","Israele wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati chotengera choti munthu sakondwera nacho.","Pakuti anakwera kunka ku Asiriya, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wake; Efuremu walembera omkonda ngati antchito.","Inde angakhale alembera mwa amitundu ndidzawasonkhanitsa tsopano; ndipo ayamba kuchepa chifukwa cha katundu wa mfumu ya akalonga.","Popeza Efuremu anachulukitsa maguwa a nsembe akuchimwako, maguwa a nsembe omwewo anamchimwitsa.","Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za chilamulo changa, koma zinayesedwa ngati chinthu chachilendo.","Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito.","Pakuti Israele waiwala Mlengi wake, namanga akachisi; ndipo Yuda wachulukitsa midzi yamalinga; koma ndidzatumizira midzi yake moto, nudzatha nyumba zake zazikulu."]