["Ndipo chopereka chake chikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng'ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema pamaso pa Yehova.","Ndipo aike dzanja lake pa mutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata cha chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira.","Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova, yotengako ku nsembe yoyamika; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,","ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.","Ndipo ana a Aroni azitenthe pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.","Ndipo chopereka chake chikakhala nkhosa kapena mbuzi, kuti ikhale nsembe yoyamika ya kwa Yehova; ingakhale yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema;","akabwera nayo nkhosa kuti ikhale chopereka chake, abwere nayo pamaso pa Yehova;","naike dzanja lake pamutu pa chopereka chake, naiphe patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira.","Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ake, mchira wamafuta wonse, atauchotsa kufupi ku fupa la msana; naichotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,","ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.","Ndipo wansembe azitenthe pa guwa la nsembe; ndicho chakudya cha nsembe yamoto ya kwa Yehova.","Ndipo chopereka chake chikakhala mbuzi, azibwera nayo pamaso pa Yehova;","naike dzanja lake pamutu pake, naiphe pa khomo la chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira.","Ndipo abwere nacho chopereka chake chotengako, ndicho nsembe yamoto ya kwa Yehova; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,","ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.","Ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe; ndizo chakudya cha nsembe yamoto ichite fungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.","Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi."]