["Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.","Pakuti mudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa Ambuye Yesu.","Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama;","yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu,","kosati m'chiliro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;","asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake m'menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni.","Pakuti Mulungu sanaitana ife titsate chidetso, koma chiyeretso.","Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.","Koma kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake;","pakutinso munawachitira ichi abale onse a m'Masedoniya lonse. Koma tikudandaulirani, abale, muchulukireko koposa,","ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;","kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.","Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.","Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu.","Pakuti ichi tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.","Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka;","pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.","Chomwecho, tonthozanani ndi mau awa."]